4 Ndidzakuyankhani,Ndi anzanu pamodzi ndi inu.
5 Yang'anani kumwamba, nimuone,Tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.
6 Ngati mwacimwa, mumcitira Iye ciani?Zikacuruka zolakwa zanu, mumcitira Iye ciani?
7 Mukakhala wolungama, mumninkhapo ciani?Kapena alandira ciani pa dzanja lanu?
8 Coipa canu cikhoza kuipira munthu wonga inu,Ndi cilungamo canu cikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.
9 Cifukwa ca kucuruka masautso anthu anapfuula,Apfuula cifukwa ca dzanja la amphamvu.
10 Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga,Wakupatsa nyimbo usiku;