9 Cifukwa ca kucuruka masautso anthu anapfuula,Apfuula cifukwa ca dzanja la amphamvu.
10 Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga,Wakupatsa nyimbo usiku;
11 Wakutilangiza ife koposa nyama za padziko,Wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?
12 Apo apfuula, koma Iye sawayankha;Cifukwa ca kudzikuza kwa anthu oipa.
13 Zedi Mulungu samvera zacabe,Ndi Wamphamvuyonse sazisamalira.
14 Inde mungakhale munena, Sindimpenya,Mlanduwo uli pamaso pace, ndipo mumlindira.
15 Ndipo tsopano popeza analibe kumzonda m'kukwiya kwace,Ndi kusamalitsa colakwa,