1 Pa icinso mtima wanga unienjemera,Nusunthika m'malo mwace.
2 Mvetsetsani cibumo ca mau ace,Ndi kugunda koturuka m'kamwa mwace.
3 Akumveketsa pansi pa thambo ponse,Nang'anipitsa mphezi yace ku malekezero a dziko lapansi.
4 Mau abuma kuitsata,Agunda ndi mau a ukulu wace,Ndipo sailetsa atamveka mau ace,