17 Kodi mudziwa umo zobvala zanu zifundira,Pamene dziko liri thuu cifukwa ca mwela?
18 Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye,Ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka?
19 Mutilangize cimene tidzanena ndi Iye;Sitidziwa kulongosola mau athu cifukwa ca mdima.
20 Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena,Kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa?
21 Ndipo tsopano anthu sakhoza kupenyerera kuunika pakunyezimira kuthambo,Ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa,
22 Kucokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira,Mulungu ali nao ukulu woopsa.
23 Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa;Koma mwa ciweruzo ndi cilungamo cocuruka samasautsa.