5 Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ace,Acita zazikuru osazidziwa ife.
6 Pakuti anena kwa cipale cofewa, Ugwe padziko.Momwemonso kwa mvula,Ndi kwa mbvumbi waukuru.
7 Atsekereza mokhomera cizindikilo dzanja la munthu ali yense,Kuti anthu onse anawalenga adziwe.
8 Pamenepo zirombo zilowa mobisalamo,Nizikhala m'ngaka mwao.
9 M'cipinda mwace muturuka kabvumvulu,Ndi cisanu cifuma kumpoto.
10 Mwa kupuma kwace apereka cipale,Ndi madzi acitando aundana.
11 Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi,Afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yace;