1 Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kabvumvulu, nati,
2 Ndani uyu adetsa uphungu,Ndi mau opanda nzeru?
3 Udzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna;Ndikufunsa, undidziwitse.
4 Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.