11 Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?
12 Kodi walamulira m'mawa ciyambire masiku ako,Ndi kudziwitsa mbanda kuca malo ace;
13 Kuti agwire malekezero a dziko lapansi,Nakutumule oipa acokeko?
14 Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa cosindikiza,Ndi zonse zibuka ngati cobvala;
15 Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.
16 Kodi unalowa magwero a nyanja?Kodi unayendayenda pozama peni peni?
17 Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe?Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?