14 Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa cosindikiza,Ndi zonse zibuka ngati cobvala;
15 Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.
16 Kodi unalowa magwero a nyanja?Kodi unayendayenda pozama peni peni?
17 Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe?Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?
18 Kodi unazindikira citando ca dziko lapansi?Fotokozera, ngati ucidziwa conse.
19 Iri kuti njira yomukira pokhala kuunika?Ndi mdima, pokhala pace pali kuti,
20 Kuti upite nao ku malire ace,Kuti uzindikire miseu ya ku nyumba yace?