2 Ndani uyu adetsa uphungu,Ndi mau opanda nzeru?
3 Udzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna;Ndikufunsa, undidziwitse.
4 Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.
5 Analemba malire ace ndani, papeza udziwa?Anayesapo cingwe cace ndani?
6 Maziko ace anakumbidwa pa ciani?Kapena anaika ndani mwala wace wa pangondya,
7 Muja nyenyezi za m'mawa zinayimba limodzi mokondwera,Ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi cimwemwe?
8 Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko,Muja idakamula ngati kuturuka m'mimba,