21 Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo,Ndi masiku ako acuruka kuwerenga kwao.
22 Kodi unalowa m'zosungiramo cipale cofewa?Kapena unapenya zosungiramo matalala,
23 Amene ndiwasungira tsiku la nsautso,Tsiku lakulimbana nkhondo?
24 Njira iri kuti yomukira pogawikana kuunika,Kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa pa dziko lapansi?
25 Ndani anacikumbira mcera cimvula,Kapena njira ya bingu la mphezi,
26 Kubvumbitsa mvula pa dziko lapanda anthu,Ku cipululu kosakhala munthu,
27 Kukhutitsa thengo la kunkhwangwala,Ndi kuphukitsa msipu?