7 Muja nyenyezi za m'mawa zinayimba limodzi mokondwera,Ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi cimwemwe?
8 Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko,Muja idakamula ngati kuturuka m'mimba,
9 Muja ndinayesa mtambo cobvala cace,Ndi mdima wa bii nsaru yace yakulunga,
10 Ndi kuilembera malire anga,Ndi kuika mipikizo ndi zitseko,
11 Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?
12 Kodi walamulira m'mawa ciyambire masiku ako,Ndi kudziwitsa mbanda kuca malo ace;
13 Kuti agwire malekezero a dziko lapansi,Nakutumule oipa acokeko?