11 Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yace njaikuru?Udzaisiyira nchito yako kodi?
12 Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako,Ndi kuzisonkhanitsira kudwale?
13 Phiko la nthiwatiwa likondwera,Koma mapiko ndi nthenga zace nzofatsa kodi?
14 Pakuti isiya mazira ace panthaka,Nimafunditsa m'pfumbi,
15 Niiwala kuti phazi lingawaphwanye,Kapena cirombo cingawapondereze.
16 Iumira mtima ana ace monga ngati sali ace;Idzilemetsa ndi nchito cabe, popeza iribe mantha;
17 Pakuti Mulungu anaimana nzeru,Ndipo sanaigawira luntha.