18 Ikafika nthawi yace, iweramuka,Iseka kavalo ndi wa pamsana pace.
19 Wampatsa kavalo mphamvu yace kodi?Wambveka pakhosi pace cenjerere cogwedezeka?
20 Wamlumphitsa kodi ngati dzombe?Ulemerero wa kumina kwace ngwoopsa.
21 Apalasa kucigwa, nakondwera nayo mphamvu yace;Aturuka kukomana nao eni zida.
22 Aseka mantha osaopsedwa,Osabwerera kuthawa lupanga.
23 Phodo likuti koco koco panthiti pace,Mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe.
24 Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka,Osaimitsika pomveka lipenga.