2 Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira,Kapena udziwa nyengo yoti ziswane?
3 Zithuntha, ziswa,Zitaya zowawa zao.
4 Ana ao akhala ojinca, akulira kuthengo,Acoka osabwerera kwa amao.
5 Ndani walola mbidzi ituruke yaufulu?Anaimasulira mbidzi nsinga zace ndani,
6 Imene ndaciyesa cipululu nyumba yace,Ndi dziko lakhulo pokhala pace?
7 Aseka phokoso la kumudzi,Osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli.
8 Poyenda ponse pamapiri mpa busa pace;Ilondola caciwisi ciri conse.