6 Imene ndaciyesa cipululu nyumba yace,Ndi dziko lakhulo pokhala pace?
7 Aseka phokoso la kumudzi,Osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli.
8 Poyenda ponse pamapiri mpa busa pace;Ilondola caciwisi ciri conse.
9 Kodi njati idzabvomera kukutumikira,Idzakhala ku codyetseramo cako kodi?
10 Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lace ilime m'mcera?Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa?
11 Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yace njaikuru?Udzaisiyira nchito yako kodi?
12 Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako,Ndi kuzisonkhanitsira kudwale?