13 Ndani adzasenda cobvala cace cakunja?Adzalowa ndani ku mizere iwiri ya mano ace?
14 Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pace?Mano ace aopsa pozungulira pao.
15 Maamba ace olimba ndiwo kudzitama kwace;Amangika pamodzi ngati okomeredwatu.
16 Alumikizana lina ndi linzace,Mphepo yosalowa pakati pao.
17 Amamatirana lina ndi linzace,Agwirana osagawanikana.
18 Pakuyetsemula ing'anipitsa kuunika,Ndi maso ace akunga zikope za m'mawa.
19 M'kamwa mwace muturuka miuni,Mbaliwali za moto zibukamo.