2 Kodi ukhoza kumanga m'mphuno ndi mlulu?Kapena kuboola nsagwada wace ndi momba?
3 Kodi idzacurukitsa mau akukupembedza?Kapena idzanena nawe mau ofatsa?
4 Kodi idzapangana ndi iwe,Kuti uitenge ikhale kapolo wako wacikhalire?
5 Kodi udzasewera nayo ngati mbalame?Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?
6 Kodi opangana malonda adzaitsatsa?Adzaigawana eni malonda?
7 Kodi udzadzaza khungu lace ndi nchetho,Kapena mutu wace ndi miomba?
8 Isanjike dzanja lako;Ukakumbukila nkhondoyi, sudzateronso.