20 M'mphuno mwace muturuka utsi,Ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi.
21 Mpweya wace uyatsa makara,Ndi m'kamwa mwace muturuka lawi la moto.
22 Kukhosi kwace kukhala mphamvu,Ndi mantha abvumbuluka patsogolo pace,
23 Nyama yace yopsapsala igwiranaIkwima pathupi pace yosagwedezeka.
24 Mtima wace ulimba ngati mwala,Inde ulimba ngati mwala wa mphero,
25 Ikanyamuka, amphamvu acita mantha;Cifukwa ca kuopsedwa azimidwa nzeru.
26 Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma;Ngakhale nthungo, kapena mubvi, kapena mkondo.