23 Nyama yace yopsapsala igwiranaIkwima pathupi pace yosagwedezeka.
24 Mtima wace ulimba ngati mwala,Inde ulimba ngati mwala wa mphero,
25 Ikanyamuka, amphamvu acita mantha;Cifukwa ca kuopsedwa azimidwa nzeru.
26 Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma;Ngakhale nthungo, kapena mubvi, kapena mkondo.
27 Citsulo iciyesa phesi,Ndi mkuwa ngati mtengo woola.
28 Mubvi suithawitsa,Miyala ya pacoponyera iisandutsa ciputu,
29 Zibonga ziyesedwa ciputu,Iseka kuthikuza kwace kwa nthungo,