28 Mubvi suithawitsa,Miyala ya pacoponyera iisandutsa ciputu,
29 Zibonga ziyesedwa ciputu,Iseka kuthikuza kwace kwa nthungo,
30 Kumimba kwace ikunga mapale akuthwa,Itasalala kuthope ngati copunthira.
31 Icititsa nthubwinthubwi pozama ngati nkhali,Isanduliza nyanja ikunge mafuta.
32 Icititsa mifunde yonyezimira pambuyo pace;Munthu akadati pozama pali ndi imvi.
33 Pa dziko lapansi palibe cina colingana nayo,Colengedwa copanda mantha.