9 Taona, ciyembekezo cako ca pa iyo cipita pacabe.Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?
10 Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?
11 Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze?Ziri zonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.
12 Sindikhala cete osachula ziwalo za ng'onayo,Ndi mbiri ya mphamvu yace, ndi makonzedwe ace okoma.
13 Ndani adzasenda cobvala cace cakunja?Adzalowa ndani ku mizere iwiri ya mano ace?
14 Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pace?Mano ace aopsa pozungulira pao.
15 Maamba ace olimba ndiwo kudzitama kwace;Amangika pamodzi ngati okomeredwatu.