1 Pamenepo Yobu anayankha Mulungu, nati,
2 Ndidziwa kuti mukhoza kucita zonse,Ndi kuti palibe coletsa colingirira canu ciri conse,
3 Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu?Cifukwa cace ndinafotokozera zimene sindinazizindikira,Zondidabwiza, zosazidziwa ine,
4 Tamveranitu, ndidzanena ine,Ndidzakufunsani, mundidziwitse.
5 Kumva ndidamva mbiri yanu,Koma tsopano ndikupenyani maso;
6 Cifukwa cace ndekha ndidzinyansa, ndi kulapaM'pfumbi ndi mapulusa.