1 Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi?Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?
2 Pakuti mkwiyo umapha wopusa,Ndi nsanje imakantha wopanda pace.
3 Ndinapenya wopusa woyala mizu;Koma pomwepo ndinatemberera pokhala pace.
4 Ana ace akhala otekeseka, Napsinjika kucipata,Wopanda wina wakuwapulumutsa.