12 Apititsa pacabe ziwembu za ocenjerera,Kuti manja ao sakhoza kucita copangana cao.
13 Akola eni nzeru m'kucenjerera kwao,Ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pacabe,
14 Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa,Nayambasa dzuwa liri pakati pamtu monga usiku.
15 Apulumutsa aumphawi ku lopangaLa kukamwa kwao, ndi ku dzanja la wamphamvu.
16 Potero aumphawi ali naco ciyembekezo,Ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.
17 Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula;Cifukwa cace usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.
18 Pakuti apweteka, namanganso mabala;Alasa, ndi manja ace omwe apoletsa.