16 Potero aumphawi ali naco ciyembekezo,Ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.
17 Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula;Cifukwa cace usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.
18 Pakuti apweteka, namanganso mabala;Alasa, ndi manja ace omwe apoletsa.
19 Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi;Cinkana mwa asanu ndi awiri palibe coipa cidzakukhudza.
20 Adzakuombola kuimfa m'njala,Ndi ku mphamvu ya lupanga m'nkhondo.
21 Udzabisikira mkwapulo wa lilime,Sudzaciopanso cikadza cipasuko.
22 Cipasuko ndi njala udzaziseka;Ngakhale zirombo za padziko osaziopa.