20 Adzakuombola kuimfa m'njala,Ndi ku mphamvu ya lupanga m'nkhondo.
21 Udzabisikira mkwapulo wa lilime,Sudzaciopanso cikadza cipasuko.
22 Cipasuko ndi njala udzaziseka;Ngakhale zirombo za padziko osaziopa.
23 Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala ya kuthengo;Ndi nyama za kuthengo zidzakhala nawe mumtendere.
24 Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere;Nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu,
25 Udzapezanso kuti mbeu zako zidzacuruka,Ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.
26 Udzafika kumanda utakalamba,Monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yace.