24 Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere;Nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu,
25 Udzapezanso kuti mbeu zako zidzacuruka,Ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.
26 Udzafika kumanda utakalamba,Monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yace.
27 Taona, ici tacifunafuna, ciri catero;Ucimvere, nucidziwire wekha.