4 Ana ace akhala otekeseka, Napsinjika kucipata,Wopanda wina wakuwapulumutsa.
5 Zokolola zao anjala azidya,Azitenga ngakhale kuminga,Ndi aludzu ameza cuma cao.
6 Pakuti nsautso siituruka m'pfumbi,Ndi mabvuto saphuka m'nthaka;
7 Koma munthu abadwira mabvuto,Monga mbaliwali zikwera ziuluzika.
8 Koma ine ndikadafuna Mulungu,Ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;
9 Amene acita zazikuru ndi zosalondoleka,Zinthu zodabwiza zosawerengeka.
10 Amene abvumbitsa mvula panthaka,Natumiza madzi paminda;