8 Koma ine ndikadafuna Mulungu,Ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;
9 Amene acita zazikuru ndi zosalondoleka,Zinthu zodabwiza zosawerengeka.
10 Amene abvumbitsa mvula panthaka,Natumiza madzi paminda;
11 Kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka,Kuti iwo a maliro akwezedwe posatekeseka.
12 Apititsa pacabe ziwembu za ocenjerera,Kuti manja ao sakhoza kucita copangana cao.
13 Akola eni nzeru m'kucenjerera kwao,Ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pacabe,
14 Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa,Nayambasa dzuwa liri pakati pamtu monga usiku.