1 Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno?Kodi masiku ace sakunga masiku a wolembedwa nchito?
2 Monga kapolo woliralira mthunzi,Monga wolembedwa nchito ayembekezera mphotho yace,
3 Momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pace.Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.
4 Ndigona pansi, ndikuti,Ndidzauka liti? koma usiku undikulira;Ndipo ndimapalapata mpaka mbanda kuca.
5 Mnofu wanga wabvala mphutsi ndi nkanambo zadothi;Khungu langa lang'ambika, nilinyansa.
6 Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,Apitirira opanda ciyembekezo.