4 Ndigona pansi, ndikuti,Ndidzauka liti? koma usiku undikulira;Ndipo ndimapalapata mpaka mbanda kuca.
5 Mnofu wanga wabvala mphutsi ndi nkanambo zadothi;Khungu langa lang'ambika, nilinyansa.
6 Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,Apitirira opanda ciyembekezo.
7 Kumbukila kuti moyo wanga ndiwo mphepo,Diso langa silidzaonanso cokoma.
8 Diso la amene andiona silidzandionanso,Maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.
9 Mtambo wapita watha,Momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.
10 Sadzabweranso ku nyumba yace,Osamdziwanso malo ace.