7 Kumbukila kuti moyo wanga ndiwo mphepo,Diso langa silidzaonanso cokoma.
8 Diso la amene andiona silidzandionanso,Maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.
9 Mtambo wapita watha,Momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.
10 Sadzabweranso ku nyumba yace,Osamdziwanso malo ace.
11 Potero sindidzaletsa pakamwa panga;Ndidzalankhula popsinjika mumzimu mwanga;Ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.
12 Ndine nyanja kodi, kapena cinjoka ca m'nyanja,Kuti Inu mundiikira odikira?
13 Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,Pogona panga padzacepsa condidandaulitsa;