24 Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.
25 Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo iye anapotoloka, nati kwa iwo.
26 Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wace ndi amace, ndi mkazi wace, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ace, inde ndi moyo wace womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.
27 Ndipo amene ali yense sasenza mtanda wace wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga,
28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza?
29 Kuti kungacitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ace, osakhoza kuimariza, anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye,
30 ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza.