7 Ndipo kodi Mulungu sadzacitira cilungamo osankhidwa ace akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?
8 Ndinena ndi inu, adzawacitira cilungamo posacedwa. Koma Mwana wa munthu pakudza Iye, vadzapeza cikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?
9 Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,
10 Anthu awiri anakwera kunka kukacisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzace wamsonkho.
11 Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, acigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;
12 ndisala cakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi lamagawo khumi la zonse ndiri nazo.
13 Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pacifuwa pace nanena, Mulungu, mundicitire cifundo, ine wocimwa.