13 Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzacita ciani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamcitira iye ulemu.
14 Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzace, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti colowa cace cikhale cathu.
15 Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha, Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawacitira ciani?
16 iye adzafika nadzaononga olima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva, anati, Musatero iail
17 Koma iye anawapenyetsa iwo, nati, Nciani ici cinalembedwa,Mwala umene anaukana omanga nyumba,Womwewu unakhala mutu wa pangondya.
18 Munthu yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha.
19 Ndipo alembi ndi ansembe akuru anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.