6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, iye analowa m'sunagoge naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lace lamanja linali lopuwala.
7 Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda iye, ngati adzaciritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze comneneza iye.
8 Koma iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lace lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.
9 Ndipo Iyeananyamuka, naimirira. Ndipo Yesuanati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kucita zabwino, kapena kucita zoipa? kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?
10 Ndipo pamene anaunguza-unguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako, Ndipo iye anatero, ndi dzanja lace lina; bwerera momwe.
11 Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzace kuti amcitire Yesu ciani.
12 Ndipo kunali masiku awa, iye anaturuka nanka kuphiri kukapemphera; nacezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.