25 Ndipo panali pakulowa Petro, Komeliyo anakomana naye, nagwa pa mapazi ace, namlambira.
26 Koma Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.
27 Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;
28 ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa;
29 cifukwa cacenso ndinadza wosakana, m'mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji?
30 Ndipo Komeliyo anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lacisanu ndi cinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wobvala cobvala conyezimira,
31 nati Komeliyo, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zacifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.