1 Ndipo kunali aneneri ndi aphunzioo ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnaba, ndi Sumeoni, wonenedwa Nigeri, ndi Lukiya wa ku Kurene, Manayeni woleredwa pamodzi ndi Herode ciwangaco, ndi Saulo.
2 Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
3 Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.
4 Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya; ndipo pocokerapo anapita m'ngalawa ku Kupro.