29 Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda.
30 Koma Mulungu anamuukitsa iye kwa akufa;
31 ndipo 1 anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza iye pokwera ku Yerusalemu kucokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumcitira umboni tsopano kwa anthu.
32 Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa 2 lonjezano locitidwa kwa makolo;
33 kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salmo laciwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.
34 Ndipo kuti anamuukitsa iye kwa akufa, wosabweranso kueibvundi, anateropo, 3 Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davine.
35 Cifukwa anenanso m'Salmo lina, 4 Simudzapereka Woyera wanu aone cibvundi.