31 ndipo 1 anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza iye pokwera ku Yerusalemu kucokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumcitira umboni tsopano kwa anthu.
32 Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa 2 lonjezano locitidwa kwa makolo;
33 kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salmo laciwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.
34 Ndipo kuti anamuukitsa iye kwa akufa, wosabweranso kueibvundi, anateropo, 3 Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davine.
35 Cifukwa anenanso m'Salmo lina, 4 Simudzapereka Woyera wanu aone cibvundi.
36 Pakutitu, Davine, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwace mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ace, naona cibvundi;
37 koma iye amene Mulungu anamuukitsa sanaona cibvundi.