38 Potero padziwike ndi inu amuna abale, 5 kuti mwa iye cilalikidwa kwa inu cikhululukiro ca macimo;
39 ndipo 6 mwa iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama kumcotsera zonse zimene simunangathe kudzicotsera poyesedwa wolungama ndi cilamulo ca Mose.
40 Cifukwa cace penyerani, kuti cingadzere inu conenedwa ndi anenenwo:
41 7 Taona ni, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;Kuti ndigwiritsa nchito Ine masikuanu,Nchito imene simudzaikhulupira wina akakuuzani.
42 Ndipo pakuturuka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.
43 Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata. Paulo ndi Bamaba; amene, polankhula nao, 8 anawaumiriza akhale m'cisomo ca Ambuye.
44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu.