40 Cifukwa cace penyerani, kuti cingadzere inu conenedwa ndi anenenwo:
41 7 Taona ni, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;Kuti ndigwiritsa nchito Ine masikuanu,Nchito imene simudzaikhulupira wina akakuuzani.
42 Ndipo pakuturuka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.
43 Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata. Paulo ndi Bamaba; amene, polankhula nao, 8 anawaumiriza akhale m'cisomo ca Ambuye.
44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu.
45 Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nacita mwano.
46 Ndipo Paulo ndi Bamaba analimbika mtima ponena, nati, 9 Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. 10 Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.