7 kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.
8 Ndipo pa Lustra panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwace, wopunduka cibadwire, amene sanayenda nthawi zonse.
9 Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi cikhulupiriro colandira naco moyo,
10 anati ndi mau akuru, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.
11 Pamene makamu anaona cimene anacita Paulo, anakweza mau ao, nati m'cinenero ca Lukaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.
12 Ndipo anamucha Bamaba, Zeu; ndi Paulo, Herme, cifukwa anali wotsogola kunena.
13 Koma wansembe wa Zeu wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.