19 Koma pamene ambuye ace anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akuru,
20 ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa abvuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda,
21 ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuicita, ndife Aroma.
22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira maraya ao; nalamulira kuti awakwapule.
23 Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.
24 Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'cipinda ca m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.
25 Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Sila analinkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;