18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, ici ciani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zacilendo, cifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.
19 Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa ciphunzitso ici catsopano ucinena iwe?
20 Pakuti ufika nazo ku makutu athu zacilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?
21 (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osacita kanthu kena koma kunena kapena kumva catsopano.)
22 Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati,Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.
23 Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Cimene mueipembedza osacidziwa, cimeneco ndicilalikira kwa inu.
24 Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba zakacisi zomangidwa ndi manja;