11 Ndipo anakhala komwe caka cimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsamau a Mulungu mwa iwo.
12 Tsono pamene Galiyo anali ciwanga ca Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye ku mpando wa ciweruziro,
13 kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana cilamulo.
14 Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pace, Galiyo anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa cosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;
15 koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi cilamulo canu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.
16 Ndipo anawapitikitsa pa mpando wa ciweruziro.
17 Ndipo anamgwira Sostene, mkuru wa sunagoge, nampanda ku mpando wa ciweruziro. Ndipo Galiyo sanasamalira zimenezi.