19 Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.
20 Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi yina yoenjezerapo, sanabvomereza;
21 koma anawatsazika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anacoka ku Efeso m'ngalawa.
22 Ndipo pamene anakoceza pa Kaisareya, anakwera nalankhulana nao Mpingo, natsikira ku Antiokeya.
23 Atakhala kumeneko nthawi, anacoka, napita pa dziko la Galatiya ndi Frugiya m'dziko m'dziko, nakhazikitsaakuphunzira onse.
24 Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lace Apolo, pfuko lace la ku Alesandreya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo.
25 Iyeyo aoaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wacangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;