20 Dzuwa lidzasanduka mdima,Ndi mweziudzasanduka mwazi,Lisanadze tsiku la Ambuye,Lalikuru ndi loonekera;
21 Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina laAmbuye adzapulumutsidwa.
22 Amuna inu Aisrayeli, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wocokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndizimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha;
23 ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampacika ndi kumupha ndi manja a anthu osayeruzika;
24 yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo.
25 Pakuti Davine anena za Iye,Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse;Cifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;
26 Mwa ici unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa;Ndipo thupi langanso lidzakhala m'ciyembekezo.