26 Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwace m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kacisi, nauza cimarizidwe ca masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.
27 Ndipo pamene masiku asanu, ndi awiri anati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kacisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,
28 napfuula, Amuna a Israyeli, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi cilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Ahelene nalowa nao m'Kacisi, nadetsa malo ana oyera.
29 Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye kuKacisi.
30 Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumturutsa m'Kacisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.
31 Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkuru wa gululo kuti m'Yerusalemumonse muli pinngu-piringu,
32 Ndipo posacedwa iye anatenga asilikari ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkuru ndi asilikari, analeka kumpanda Paulo.