28 napfuula, Amuna a Israyeli, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi cilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Ahelene nalowa nao m'Kacisi, nadetsa malo ana oyera.
29 Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye kuKacisi.
30 Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumturutsa m'Kacisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.
31 Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkuru wa gululo kuti m'Yerusalemumonse muli pinngu-piringu,
32 Ndipo posacedwa iye anatenga asilikari ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkuru ndi asilikari, analeka kumpanda Paulo.
33 Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?
34 Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.